14/07/2022
*Rhapsody of Realities*
*By Pastor Chris*
*(Chichewa Version)*
*lachinayi 14, July 2022*
*MOYO WOSATHA UNATIBWERETSERA KUSAKALAMBA*
Atate wanu Abrahamu anakondwera
kuona tsiku langa; ndipo anaona
nasangalala. Ayuda pamenepo anati kwa
Iye, Simunafikire zaka makumi asanu,
ndipo munaona Abrahamu kodi? Yesu
anati kwa iwo, Indetu, indetu, ndinena
kwa inu, asanayambe kukhala Abrahamu
ndipo Ine ndilipo
*(Yohane 8:56-58).*
Ndi mawu awa akuti - “ Asanayambe kukhala
Abrahamu ndipo Ine ndilipo...” -Ambuye
Yesu adalengeza zakusakalamba. Kusakalamba
kumatanthauza moyo wa chitukuko chosatha,
komwe mumakula popanda kukalamba. Ndi moyo
wopanda mathero, wopanda chivundi komanso
wosawonongeka. Pamene mudabadwa mwatsopano,
mudalandira moyo wamuyaya monga Yesu ndipo
mudabweretsedwa ku moyo wosakalamba.
https://chat.whatsapp.com/GebTAZOadei6pJNA9apS61
Pokamba za moyo wosatha, Yohane adati:
“Chimene chinaliko kuyambira pachiyambi,
chimene tidachimva, chimene tidachiona m’maso
mwathu, chimene tidachipenyerera, ndipo manja
athu adachigwira cha Mau a moyo, (ndipo moyowo
unaonekera, ndipo tidaona, ndipo tichita umboni,
ndipo tikulalikirani moyo wosathawo, umene unali
kwa Atate, nuonekera kwa ife)” (1 Yohane 1:1-2).
Chifukwa chimene Zinawonetsedwera ndichakuti
ifeyo tikakhale nawo komanso tidzikhala ndi moyo
womwewo. Mukamawerenga Malemba ndikuwona
zowonadi zoterezi, mumawona mawonekedwe anu
enieni ndipo mungathe kudziwa za momwe moyo
wanu uyenera kukhalira.
Tsopano pakuti mudabadwa mwatsopano,
mudabadwira mwa Mulungu, m’moyo wosatha!
Kukhala m’Mawu a Mulungu, ndi mwa Khristu, ndiko
kukhala m’moyo wosatha. Uwu ndi moyo umene muli
nawo. Inu muli mwa Khristu; Ndiye malo anu atsopano.
Sindinu wa dziko lino lapansi. Chomcho, yambani
kukhala ndi moyo wanu wosakalamba.
*PEMPHERO LOVOMEREZA*
Ndine chilungamo cha Mulungu mwa Khristu Yesu
ndipo ndiri ndi Moyo wa Mulungu mwa ine. Mzimu
wanga, moyo ndi thupi zapatsidwa moyo kudzera
m’mphamvu komanso zotsatira za chilungamo ndi
chidzalo cha moyo womwe ndidalandira kudzera
mu Uthenga Wabwino. Ndikuyenda mu zenizeni
za cholowa changa chaumulungu mwa Khristu,
kuzindikira chisomo chake ndi kupezeka Kwake
kosangalatsa m’moyo wanga, m’Dzina la Yesu.
Amen.
*WERENGANINSO:*
Yohane 11:25-26
Aroma 8:11
1 Yohane 5:11-12 NIV
*Ndondomeko Yowerenga Baibulo Chaka Chimodzi :*
*Ndondomeko Yowerenga Baibulo Zaka Ziwiri :*
Machitidwe 22:22-23:1-11 & Yobu 36-39
Agalatiya 4:1-11 & Yesaya 34
For your loved ones who have *visual challenges*, those who have *difficult reading* and those who just *enjoying listening* to the Rhapsody Message, we now have the Rhapsody in *Audio format*, in the following languages, in our Groups :
*English, Xhosa, Shona, Ndebele, Setswana, Sesotho and Zulu.*
*PEMPHERO LA CHIPULUMUTSO*
Tikukhulupirira kuti mwadalitsika ndi bukuli. Ndipo tikukumemani kuti mumlandire yesu khristu kuti akhale mbuye wa moyo wanu popemphera pemphero ili:
*“Ambuye mulungu, ndi mtima wanga wonse, ndikukhulupilira mwa yesu khristu, mwana wa mulungu wamoyo. Ndikukhulupilira kuti iye adandifera ine ndipo mulungu adamuukitsa kwa akufa. ndikukhulupilira kuti iye ali ndi moyo lero. Ndikuvomereza ndi pakamwa panga kuti yesu khristu ndi ambuye a moyo wanga kuyambira lero. Kudzera mwa iye ndi mwa dzina lake, ndiri ndi moyo wosatha; ndabadwanso mwatsopano. Zikomo ambuye, populumutsa moyo wanga! ndine mwana wa mulungu tsopano. Halleluiah!”*
Mwachita bwino! Ndinu mwana wa mulungu tsopano.
..
*GREAT NEWS*
You can now receive the *Rhapsody of Realities Daily Devotional* messages, in your *mother tongue*, every morning on your phone or device, including *English Rhapsody* and *Teevo*
Currently we have the following *African Languages* available in our Groups (in Alphabetic Order):
*Afrikaans, Chichewa, Ndebele, Nyanja, Sesotho, Setswana, Shona, SiSwati, Xhosa, and Zulu*; and counting!
Also *invite* your friends, family and colleagues, to join the Group. Send them a copy of this Rhapsody, with the *JOIN the Group* Link.
*Click Here – to JOIN Our Groups*
https://chat.whatsapp.com/GebTAZOadei6pJNA9apS61
WhatsApp Group Invite